Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 15:46-56 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

46. Koma cauzimu siciri coyamba, koma cacibadwidwe; pamenepo cauzimu.

47. 13 Munthu woyambayo ali wapansi, wanthaka. Munthu waciwiri ali wakumwamba.

48. 14 Monga wanthakayo, ateronso anthaka; ndi monga wakumwamba, ateronso akumwamba.

49. Ndipo 15 monga tabvaia fanizo la wanthakayo, tidzabvalanso fanizo la wakumwambayo.

50. Koma ndinena ici, abale, kuti 16 thupi ndi mwazi sizingathe kulowa Ufumu wa Mulungu; kapena cibvundi sicilowa cisabvundi.

51. Taonani, ndikuuzani cinsinsi; 17 sitidzagona tonse, koma tonse tidzasandulika,

52. m'kamphindi, m'kutwanima kwa diso, pa lipenga lotsiriza; pakuti 18 lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osabvunda, ndipoife tidzasandulika.

53. Pakuti cobvunda ici ciyenera kubvala cisabvundi, ndi 19 caimfa ici kubvala cosafa.

54. Ndipo pamene cobvunda ici cikadzabvala cisabvundi ndi caimfa ici cikadzabvala cosafa, pamenepo padzacitika mau olembedwa, 20 Imfayo yamezedwa m'cigonjetso.

55. 21 Imfawe, cigonjetso cako ciri kuti? Imfawe, mbola yako iri kuti?

56. Koma mbola ya imfa ndiyo ucimo; koma 22 mphamvu ya ucimo ndiyo cilamulo:

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 15