36. Wopusa iwe, 8 cimene ucifesa wekha sieikhalitsi'dwanso camoyo, ngati sicifa;
37. ndipo cimene ufesa, sufesa thupi limene lidzakhala, koma mbeu yokhakapenaya tirigu kapena ya, mtundu wina;
38. koma Mulungu iaipatsa thupi mongaafuna; ndi, kwa mbeu yonse thupi lace lace.
39. Nyama yonse siiri imodzimodzi; koma yinandi Ya anthu, ndi yina ndiyo nyama ya zoweta, ndi yina ndiyo nyama ya mbalame, ndi yina ya nsomba.
40. Palinso matupi am'mwamba, ndi matupi apadziko: koma ulemerero wa lam'mwamba ndi wina, ndi ulemerero wa lapadziko ndi winanso.
41. Kuli ulemerero wa dzuwa, ndi ulemerero wina wa mwezi, ndi ulemerero wina wa nyenyezi; pakuti nyenyezi isiyana ndi nyenyezi m'ulemerero.
42. 9 Comweconso kudzakhala kuuka kwa akufa. Lifesedwa m'cibvundi, liukitsidwa m'cisabvundi;
43. 10 lifesedwa m'mnyozo, liukitsidwa m'ulemerero; lifesedwa m'cifoko, liukitsidwa mumphamvu;
44. lifesedwa thupi Iacibadwidwe, liukitsidwa thupi lauzimu. Ngati pali thupi Iacibadwidwe, palinso lauzimu.
45. Koteronso kwalembedwa, 11 Munthu woyamba, Adamu, anakhala mzimu wamoyo. 12 Adamu wotsirizayo anakhala mzimu wakulenga moyo.