Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 15:15-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndiponso ife tipezedwa mboni zonama za Mulungu; cifukwa n tinacita umboni kunena za Mulungu kuti anaukitsa Kristu; amene sanamuukitsa, ngati kuli tero kuti akufa saukitsidwa,

16. Pakuti ngati akufa saukitsidwa, Kristunso sanaukitsidwa;

17. ndipo ngati Kristu sanaukitsidwa, cikhulupiriro canu ciri copanda pace; muli cikhalire m'macimo anu.

18. Cifukwa cace iwonso akugona mwa Kristu anatayika.

19. Ngati tiyembekezera Kristu m'moyo uno wokha, tiri ife aumphawi oposa a anthu onse,

20. Koma tsopano Kristu waukitsidwa kwa akufa, cipatso coundukula ca iwo akugona.

21. Pakuti monga imfa inadza mwa munthu, kuuka kwa akufa kunadzanso mwa munthu.

22. Pakuti mongamwa Adamu onse amwalira, coteronso mwa Kristu onse akhalitsidwa ndi moyo.

23. Koma yense m'dongosolo lace la iye yekha, cipatso coundukula Kristu, pomwepo iwo a Kristu, pa kubwera kwace.

24. Pomwepo pali cimariziro, pamene adzapereka ufumu kwa Mulungu, ndiye Atate, atatha kuthera ciweruzo conse, ndi ulamuliro wonse, ndi mphamvu yomwe.

25. Pakuti ayenera kucita ufumu kufikira ataika adani onse pansi pa mapazi ace.

26. Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.

27. Pakuti Iye anagonjetsa zonse pansi pa mapazi ace. Koma pamene anena kutizonse zagonjetsedwa, kuzindikirika kuti sawerengapo Iye amene anagonjetsa zonsezo kwa Iye.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 15