Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 14:6-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Koma tsopano, abale, ngati ndidza kwa inu ndi kulankhula malilime, ndikaku, pindulitsani ciani, ngati sindilankhui landi inu kapena m'bvumbulutso, kapena m'cidziwitso, kapena m'cinenero, kapena m'ciphunzitsot

7. Ngakhale zinthu zopanda moyo, zopereka mau, ngati toliro, kapena ngoli, ngati sizisiyanitsa maliridwe, cidzazindikirikabwanji cimene ciombedwa kapena kuyimbidwa?

8. Pakuti ngad Lipenga lipereka mao osazindikirika, adzadzikonzera ndani kunkhondo?

9. Momwemonso inu ngati mwa lilime simupereka mau omveka bwino, kudzazindikirika bwanji cimene cilankhulidwa? Pakuti mudzakhala olankhula kumlengalenga.

10. Iripo, kaya, mitundu yambiri yotere ya mau pa dziko lapansi, ndipo palibe kanthu kasowa mau.

11. Cifukwa cace, ngati sindidziwa mphamvu ya mauwo ndidzakhala kwa iye wolankhulayo wakunja, ndipo wolankhulayo adzakhala wakunja kwaine.

12. Momwemo inunso, popeza muli ofunits its a mphatso zauzimu, funani kuti mukacuruke kukumangirira kwa Mpingo,

13. Cifukwa cace wolankhula lilime, apemphere kuti amasule.

14. Pakuti ngati ndipemphera m'lilime, mzimu wanga upemphera, koma cidziwitso canga cikhala cosabala kanthu.

15. Kuli ciani tsono? Ndidzapemphera ndi mzimu, koma ndidzapempheranso ndi cidziwitso canga; ndidzayimba ndi mzimu, koma ndidzayimbanso ndi cidziwitso.

16. Cifukwa ngati udalitsa ndi mzimu, nanga iye wakukhala wosaphunzira adzati Amen bwanji, pa kuyamika kwako, popeza sadziwa cimene unena?

17. Pakutitu iwe uyamika bwino, koma winayo samangiriridwa.

18. Ndiyanillca Mulungu kuti ndilankhula malilime koposa inu nonse;

19. koma mu Mpingo ndifuna kulankhula mau asanu ndi cidziwitso canga, kutinso ndikalangize ena, koposa kulankhula mau zikwi m'lilime.

20. Abale, musakhale ana m'cidziwitso, koma m'coipa khalani makanda, koma m'cidziwitso akulu misinkhu.

21. Kwalembedwa m'cilamulo, Ndi anthu amalilime ena ndipo ndi milomo yina ndidzalankhula nao anthu awa; ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye.

22. Cotero malilime akhala ngati cizindikilo, si kwa iwo akukhulupira, koma kwa iwo osakhulupira; koma kunenera sikuli kwa iwo osakhulupira, koma kwa two amene akhulupira.

23. Cifukwa cace, ngati Mpingo wonse akasonkhane pamodzi, ndi onse akalankhule malilime, ndipo akalowemo anthu osaphunzira kapena osakhulupira, kodi sadzanena kuti mwayaruka?

24. Koma ngati onse anenera, ndipo alowamo wina wosakhulupirira kapena wosaphunzira, atsutsidwa ndi onse; aweruzidwa ndi onse;

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 14