Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 14:30-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. Koma ngati kanthu kabvumbulutsidwa kwa wina wakukhalapo, akhale cete woyambayo.

31. Pakuti mukhoza nonse kunenera mmodzi mmodzi, kuti onse aphunzire, ndi onse afulumidwe;

32. ndipo mizimu ya aneneri imvera aneneri;

33. pakuti Mulungu sali Mulungu wa cisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima.

34. Akazi akhale cete m'Mipingo. Pakuti vsikuloledwa kwa iwo kulankhula, Koma akhale omvera, mongansocilamulo cmena,

35. Koma ngati afuna kuphunzirakanthu afunseamuna ao aiwo okha kwao; pakuti kunyazitsa mkazi kulankhula mu Mpingo.

36. Kodi mau a Mulungu anatutuka kwa iw? kapena anafika kwa inu nokha?

37. Ngatiwinaayesa kuti ali mneneri, kapena wauzimu; azindikire kuti zimene ndilemba kwa inu ziri lamulo la Ambuye,

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 14