Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 14:18-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndiyanillca Mulungu kuti ndilankhula malilime koposa inu nonse;

19. koma mu Mpingo ndifuna kulankhula mau asanu ndi cidziwitso canga, kutinso ndikalangize ena, koposa kulankhula mau zikwi m'lilime.

20. Abale, musakhale ana m'cidziwitso, koma m'coipa khalani makanda, koma m'cidziwitso akulu misinkhu.

21. Kwalembedwa m'cilamulo, Ndi anthu amalilime ena ndipo ndi milomo yina ndidzalankhula nao anthu awa; ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye.

22. Cotero malilime akhala ngati cizindikilo, si kwa iwo akukhulupira, koma kwa iwo osakhulupira; koma kunenera sikuli kwa iwo osakhulupira, koma kwa two amene akhulupira.

23. Cifukwa cace, ngati Mpingo wonse akasonkhane pamodzi, ndi onse akalankhule malilime, ndipo akalowemo anthu osaphunzira kapena osakhulupira, kodi sadzanena kuti mwayaruka?

24. Koma ngati onse anenera, ndipo alowamo wina wosakhulupirira kapena wosaphunzira, atsutsidwa ndi onse; aweruzidwa ndi onse;

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 14