Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 14:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tsatani cikondi; koma funitsitsani mphatsozauzimu, koma koposa kuti mukanenere.

2. Pakuti iye wakulankhula lilime salankhula ndi anthu, koma ndi Mulungu; pakuti palibemunthu akumva; koma mumzimu alankhula zinsinsi.

3. Koma iye wakunenera alankhula ndi anthu comangirira ndi colimbikitsa, ndi cosangalatsa,

4. Iye wakulankhula lilime, adzimangirira yekha, koma iye wakunenera amangirira Mpingo.

5. Ndipo ndifuna inu nonse mula'nkhule malilime, koma makamaka kuti mukanenere; ndipo wakunenera aposa wakulankhula malilime, akapanda kumasulira, kuti Mpingo ukalandire comangirira.

6. Koma tsopano, abale, ngati ndidza kwa inu ndi kulankhula malilime, ndikaku, pindulitsani ciani, ngati sindilankhui landi inu kapena m'bvumbulutso, kapena m'cidziwitso, kapena m'cinenero, kapena m'ciphunzitsot

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 14