1. Tsatani cikondi; koma funitsitsani mphatsozauzimu, koma koposa kuti mukanenere.
2. Pakuti iye wakulankhula lilime salankhula ndi anthu, koma ndi Mulungu; pakuti palibemunthu akumva; koma mumzimu alankhula zinsinsi.
3. Koma iye wakunenera alankhula ndi anthu comangirira ndi colimbikitsa, ndi cosangalatsa,