Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 12:7-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Koma kwa yense kwapatsidwa maonekedwe a Mzimu kuti apindule nao.

8. Pakuti kwa mmodzi kwapatsidwa mwa Mzimu mau a nzeru; koma kwa mnzace mau a cidziwitso, monga mwa Mzimu yemweyo:

9. kwa wina cikhulupiriro, mwa Mzimu yemweyo; ndi kwa wina mphatso za maciritso, mwa Mzimu mmodziyo;

10. ndi kwa wina macitidwe a mphamvu; ndi kwa wina cinenero; ndi kwa wina cizindikiro ca mizimu; kwa wina malilime a mitundu mitundu; ndi kwa wina mamasulidwe a malilime.

11. Koma zonse izi acita Mzimu mmodzi yemweyo, nagawira yense payekha monga afuna.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 12