Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 12:26-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Ndipocingakhale ciwalo cimodzi cimva cowawa, ziwalo zonse zimva pamodzi; cingakhale cimodzi cilemekezedwa, ziwalo zonse zikondwera naco pamodzi,

27. Koma inundinu thupi la Kristu, ndi ziwalo, yense pa yekha.

28. Ndipotu Mulunguanailea ena m'Eklesia, poyamba arumwi, aciwiri aneneri, acitatu aphunzitsi, pamenepo zozizwa, pomwepo mphatso zamaciritso, mathandizo, maweruziro, malilime a mitundu mitundu.

29. Kodi ali onse atumwi? Ali aneneri onse kodi? Ali aphunzitsi onse? Ali onse ocita zozizwa?

30. Ali nazo mphatso za maciritso onse kodi? Kodi onse alankhula ndi malilime? Kodi onse amasulira mau?

31. Koma funitsitsani mphatso zoposa. Ndipo ndikuonetsani njira yokoma yoposatu.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 12