Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 12:18-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Koma tsopano, Mulungu anaika ziwalo zonsezo m'thupi, monga anafuna.

19. Koma ngati zonse zikadakhala ciwalo cimodzi, likadakhala kuti thupi?

20. Kama tsopano pali ziwalo zambiri, kama thupi limodzi.

21. Ndipo dise silingathe kunena kwa dzanja, Sindikufuna iwe, kapenanso mutu kwa mapazi, Sindikufunani inu.

22. Koma makamakatu ziwalozo zoyesedwa zofoka m'thupi, zifunika;

23. ndipo zimene tiziyesa Zocepa ulemum'thupi, pa izi tiika ulemu wocuruka woposa; ndi zinthu zosakoma zikhala naco cokometsera coposa,

24. Koma zokoma zathu ziribe kusowa; koma Mulungu analumikizitsa thupi, napatsa ulemu wocuruka kwa cosowaco; kuti kusakhale cisiyano m'thupi;

25. koma kuti ziwalo zifanane ndi kusamalana cinandicinzace,

26. Ndipocingakhale ciwalo cimodzi cimva cowawa, ziwalo zonse zimva pamodzi; cingakhale cimodzi cilemekezedwa, ziwalo zonse zikondwera naco pamodzi,

27. Koma inundinu thupi la Kristu, ndi ziwalo, yense pa yekha.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 12