Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 12:16-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo ngati khutu likati, Popeza sindiri diso, sindiri wa thupi; kodi siliri la thupi cifukwa ca ici?

17. Ngati thupi lonse likadakhala diso, kukadakhala kuti kununkhiza?

18. Koma tsopano, Mulungu anaika ziwalo zonsezo m'thupi, monga anafuna.

19. Koma ngati zonse zikadakhala ciwalo cimodzi, likadakhala kuti thupi?

20. Kama tsopano pali ziwalo zambiri, kama thupi limodzi.

21. Ndipo dise silingathe kunena kwa dzanja, Sindikufuna iwe, kapenanso mutu kwa mapazi, Sindikufunani inu.

22. Koma makamakatu ziwalozo zoyesedwa zofoka m'thupi, zifunika;

23. ndipo zimene tiziyesa Zocepa ulemum'thupi, pa izi tiika ulemu wocuruka woposa; ndi zinthu zosakoma zikhala naco cokometsera coposa,

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 12