Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 11:8-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Pakuti mwamuna sakhala wa kwa mkazi; koma mkazi wa kwa mwamuna;

9. pakutinso mwamuna sanalengedwa cifukwa ca mkazi;

10. koma mkazi cifukwa ca mwamuna; cifukwa ca ici mkazi ayenera kukhala nao ulamuliro pamutu pace, cifukwa ca angelo.

11. Komanso mkazi sakhala wopanda mwamuna, kapena mwamuna wopanda mkazi, mwa Ambuye.

12. Pakuti monga mkazi aliwa kwa mwamuna, comweconso mwamuna ali mwa mkazi; koma zinthu zonse ziri za kwa Mu, lungu.

13. Lingirirani mwa inu nokha: Kodi nkuyenera kuti apemphere kwa Mulungu, wosapfunda mutu?

14. Kodi ubadwidwe womwe sutiphunzitsa kuti ngati mwamuna aweta tsitsi cimnyozetsa iye?

15. Koma ngati mkazi aweta tsitsi, kuli ulemerero kwa iye; pakuti tsitsi lace lapatsidwa kwa iye ngati cophimba.

16. Koma akaoneka wina ngati wotetana, tiribe makhalidwe otere, kapena ife, kapena Eklesia wa Mulungu.

17. Koma pakulalikira ici sinditama inu, popeza simusonkhanira cokoma, koma coipa.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 11