Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 11:25-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Koteronso cikho, citatha cakudya, ndi kuti, Cikho ici ndi pangano latsopano m'mwazi wanga; citani ici, nthawi zonse mukamwa, cikhale cikumbukilo canga,

26. Pakuti nthawi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera cikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza iye.

27. Cifukwa cace yense amene akadyamkate, kapena akamwera cikho ca Ambuye kosayenera, adzakhala wocimwira thupi ndi mwazi wa Ambuye.

28. Koma munthu adziyese yekha, ndi kotero adye mkate, ndi kumwera cikho.

29. Pakuti iye wakudya ndi wakumwa, adya namwa ciweruziro kwa iye yekha, ngati sazindikira thupilo.

30. Cifukwa cace ambiri mwa inu afoka, nadwala, ndipo ambiri agona.

31. Koma ngati tikadadzizindikira tokha sitikadaweruzidwa.

32. Koma poweruzidwa, tilangidwa ndi Ambuye, kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi dziko lapansi.

33. Cifukwa cace, abale anga, posonkhanira kudya, lindanani.

34. Ngati wina ali ndi njala adye-kwao; kuti mungasonkhanire kwa ciweruziro. Koma zotsalazo nelidzafotokoza pakudza ine.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 11