Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 11:21-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. pakuti pakudyaku yense athanga watenga mgonero wace wa yekha, ndipo wina ali ndi njala, ndi wina aledzera.

22. Nanga mulibe nyumba za kudyeramo ndi kumweramo? Kapena kodi munyoza Eklesia wa Mulungu, ndi kunyoza iwo amene alibe kanthu? Ndidzanena ciani kwa inu? Kodi ndidzatama inu m'menemo? Sindikutamani.

23. Pakuti ine ndinalandira kwa Ambuye, cimenenso ndinapereka kwainu, kuti Ambuye Yesu usikuuja anaperekedwa, anatenga mkate;

24. ndipo m'mene adayamika, ananyema, nati, ici ndi thupi langa la kwa inu; citani ici cikhale cikumbukilo canga.

25. Koteronso cikho, citatha cakudya, ndi kuti, Cikho ici ndi pangano latsopano m'mwazi wanga; citani ici, nthawi zonse mukamwa, cikhale cikumbukilo canga,

26. Pakuti nthawi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera cikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza iye.

27. Cifukwa cace yense amene akadyamkate, kapena akamwera cikho ca Ambuye kosayenera, adzakhala wocimwira thupi ndi mwazi wa Ambuye.

28. Koma munthu adziyese yekha, ndi kotero adye mkate, ndi kumwera cikho.

29. Pakuti iye wakudya ndi wakumwa, adya namwa ciweruziro kwa iye yekha, ngati sazindikira thupilo.

30. Cifukwa cace ambiri mwa inu afoka, nadwala, ndipo ambiri agona.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 11