Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 11:15-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Koma ngati mkazi aweta tsitsi, kuli ulemerero kwa iye; pakuti tsitsi lace lapatsidwa kwa iye ngati cophimba.

16. Koma akaoneka wina ngati wotetana, tiribe makhalidwe otere, kapena ife, kapena Eklesia wa Mulungu.

17. Koma pakulalikira ici sinditama inu, popeza simusonkhanira cokoma, koma coipa.

18. Pakutitu poyamba posonkhana inu mu Mpingo, ndimva kuti pakhala malekano mwa inu; ndipo ndibvomereza penapo.

19. Pakuti kuyenera kuti pakhale mipatuko mwa inu, kuti iwo obvomerezedwa aonetsedwemwa inu.

20. Cifukwa cace, pakusonkhana inu pamodzi sikutheka kudya mgonero wa Ambuye;

21. pakuti pakudyaku yense athanga watenga mgonero wace wa yekha, ndipo wina ali ndi njala, ndi wina aledzera.

22. Nanga mulibe nyumba za kudyeramo ndi kumweramo? Kapena kodi munyoza Eklesia wa Mulungu, ndi kunyoza iwo amene alibe kanthu? Ndidzanena ciani kwa inu? Kodi ndidzatama inu m'menemo? Sindikutamani.

23. Pakuti ine ndinalandira kwa Ambuye, cimenenso ndinapereka kwainu, kuti Ambuye Yesu usikuuja anaperekedwa, anatenga mkate;

24. ndipo m'mene adayamika, ananyema, nati, ici ndi thupi langa la kwa inu; citani ici cikhale cikumbukilo canga.

25. Koteronso cikho, citatha cakudya, ndi kuti, Cikho ici ndi pangano latsopano m'mwazi wanga; citani ici, nthawi zonse mukamwa, cikhale cikumbukilo canga,

26. Pakuti nthawi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera cikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza iye.

27. Cifukwa cace yense amene akadyamkate, kapena akamwera cikho ca Ambuye kosayenera, adzakhala wocimwira thupi ndi mwazi wa Ambuye.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 11