Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 10:21-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Simungathe kumwera cikho ca Ambuye, ndi cikho ca ziwanda; simungathe kulandirako ku gome la Ambuye, ndi ku gome la ziwanda.

22. Kapena kodi ticititsa nsanje Ambuye? Kodi mphamvu zathu ziposa iye?

23. Zinthu zonse ziloleka; koma sizipindula zonse. Zinthu zonse ziloleka; koma sizimanga zonse.

24. Munthu asafune zace za iye yekha, kama za mnzace.

25. Conse cogulitsidwa pa msika wa nyama, mudye, osafunsa kanthu cifukwa ca cikumbu mtima;

26. pakuti dziko lapansi liri la Ambuye, ndi kudzala kwace.

27. Ngati wina wa osakhulupira akuitanani, ndipo mufuna kupita; mudye comwe ciikidwa kwa inu, osafunsa kanthu, cifukwa ca cikumbu mtima.

28. Koma ngati wina akati kwa inu, Yoperekedwa nsembe iyi, musadye, cifukwa ca iyeyo wakuuza, ndi cifukwa ca cikumbu mtima.

29. Ndinena cikumbu mtima, si ca iwe mwini, koma ca winayo; 1 pakuti ufulu wanga uyesedwa ninji ndi cikumbu mtima ca wina?

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 10