Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 10:20-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Koma nditi kuti zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziwanda; ndipo sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziwanda.

21. Simungathe kumwera cikho ca Ambuye, ndi cikho ca ziwanda; simungathe kulandirako ku gome la Ambuye, ndi ku gome la ziwanda.

22. Kapena kodi ticititsa nsanje Ambuye? Kodi mphamvu zathu ziposa iye?

23. Zinthu zonse ziloleka; koma sizipindula zonse. Zinthu zonse ziloleka; koma sizimanga zonse.

24. Munthu asafune zace za iye yekha, kama za mnzace.

25. Conse cogulitsidwa pa msika wa nyama, mudye, osafunsa kanthu cifukwa ca cikumbu mtima;

26. pakuti dziko lapansi liri la Ambuye, ndi kudzala kwace.

27. Ngati wina wa osakhulupira akuitanani, ndipo mufuna kupita; mudye comwe ciikidwa kwa inu, osafunsa kanthu, cifukwa ca cikumbu mtima.

28. Koma ngati wina akati kwa inu, Yoperekedwa nsembe iyi, musadye, cifukwa ca iyeyo wakuuza, ndi cifukwa ca cikumbu mtima.

29. Ndinena cikumbu mtima, si ca iwe mwini, koma ca winayo; 1 pakuti ufulu wanga uyesedwa ninji ndi cikumbu mtima ca wina?

30. Ngati ine ndilandirako mwacisomo, ndinenezedwa bwanji cifukwa ca ici cimene ndiyamikapo?

31. Cifukwa cace 2 mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale mucita kanthu kena, citani zonse ku ulemerero wa Mulungu.

32. 3 Khalani osakhumudwitsa, kapena Ayuda, kapena Ahelene, kapena Mpingo wa Mulungu;

33. monga 4 inenso ndikodweretsa onse m'zinthu zonse, wosafuna cipindulo canga, koma ca unyinjiwo, kuti apulumutsidwe.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 10