1. Pakuti sindifuna, kuti mukhale osadziwa, abale, kuti makolo athu onse anali pansi pa mtambo, naoloka nyanja onse;
2. nabatizidwa onse kwa Mose, mumtambo, ndi m'nyanja,
3. nadya onse cakudya cauzimu cimodzimodzi;
4. namwa onse cakumwa cauzimu cimodzimodzi; pakuti anamwa mwa thanthwe lauzimu lakuwatsata; koma thanthwelo ndiye Kristu.
5. Koma ocuruka a iwo Mulungu sanakondwera nao; pakuti anamwazika m'cipululu.