1. Pakuti sindifuna, kuti mukhale osadziwa, abale, kuti makolo athu onse anali pansi pa mtambo, naoloka nyanja onse;
2. nabatizidwa onse kwa Mose, mumtambo, ndi m'nyanja,
3. nadya onse cakudya cauzimu cimodzimodzi;
4. namwa onse cakumwa cauzimu cimodzimodzi; pakuti anamwa mwa thanthwe lauzimu lakuwatsata; koma thanthwelo ndiye Kristu.
5. Koma ocuruka a iwo Mulungu sanakondwera nao; pakuti anamwazika m'cipululu.
6. Koma zinthu izi zinacitika, zikhale zoticenjeza ife, kuti tisalakalake zoipa ife, monganso iwowo analakalaka.
7. Kapena musakhale opembedza mafano, monga ena a iwo, monga kwalembedwa, Anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nanyamuka kusewera.
8. Kapena tisacite dama monga ena a iwo anacita dama, nagwa tsiku limodzi zikwi makumi awiri ndi zitatu.
9. Kapena tisayese Ambuye, monga ena a iwo anayesa, naonongeka ndi njoka zija.
10. Kapena musadandaula, monga ena a iwo anadandaula, naonongeka ndi woonongayo.