Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 1:20-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ali kuti wanzeru? Mlembi ali kuti? Ali kuti wotsutsana wa nthawi ya pansi pano? Kodi Mulungu sanaipusitsa nzeru ya dziko lapansi?

21. Pakuti popeza m'nzeru ya Mulungu dziko lapansi, mwa nzeru yace, silinadziwa Mulungu, cidamkonda Mulungu kupulumutsa okhulupirawo mwa copusa ca kulalikira.

22. Ndipo popeza Ayuda afunsa zizindikilo, ndi Ahelene atsata nzeru:

23. koma ife tilalikira Kristu wopacikidwa, kwa Ayudatu cokhumudwitsa, ndi kwa amitundu cinthu copusa;

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 1