Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 1:10-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Koma ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti munene cimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mu mtima womwewo ndi m'ciweruziro comweco.

11. Pakuti zinamveka kwa ine za inu, abale anga, ndi iwo a kwa Kloe, kuti pali makani pakati pa inu.

12. Koma ici ndinena, kuti yense wa inu anena, Ine ndine wa Paulo; koma ine wa Apolo; koma ine wa Kefa; koma ine wa Kristu.

13. Kodi Kristu wagawika? Kodi Paulo anapacikidwa cifukwa ca inu? Kapena kodi munabatizidwa m'dzina la Paulo?

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 1