Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 1:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. PAULO, woitanidwa akhale mtumwi wa Yesu Kristu mwa cifuniro ca Mulungu, ndi Sositene mbaleyo,

2. kwa Mpingo wa Mulungu wakukhala m'Korinto, ndiwo oyeretsedwa mwa Kristu Yesu, oitanidwa akhale oyera mtima, pamodzi ndi onse akuitana pa dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, m'malo monse, ndiye wao, ndi wathu:

3. Cisomo kwa inu ndi mtendere zocokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Kristu.

4. Ndiyamika Mulungu wanga nthawi yonse kaamba ka inu, cifukwa ca cisomo ca Mulungu cinapatsidwa kwa inu mwa Kristu Yesu;

5. kuti m'zonse muoalemezedwa mwa iye, m'mau onse, ndi cidziwitso conse;

6. mongaumboni wa Kristu unakhazikika mwa inu;

7. kotero kuti sicikusowani inu caufuru ciri conse; pakulindira inu bvumbulutso la Ambuye wathu Yesu Kristu;

8. amenenso adzakukhazikitsani inu kufikira cimariziro, kuti mukhale opanda cifukwa m'tsiku la Ambuye: wathu Yesu Kristu.

9. Mulungu ali, wokhulupirika amene munaitanidwa mwa iye, ku ciyanjano ca Mwana wace Yesu Kristu, Ambuye wathu.

10. Koma ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti munene cimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mu mtima womwewo ndi m'ciweruziro comweco.

11. Pakuti zinamveka kwa ine za inu, abale anga, ndi iwo a kwa Kloe, kuti pali makani pakati pa inu.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 1