Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 9:9-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; pfuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini cipulumutso; wofatsa ndi wokwera pa buru, ndi mwana wamphongo wa buru.

10. Ndipo ndidzaononga magareta kuwacotsa m'Efraimu, ndi akavalo kuwacotsa m'Yerusalemu; ndi uta wa nkhondo udzaonongeka; ndipo adzanena zamtendere kwa amitundu; ndi ufumu wace udzakhala kuyambira kunyanja kufikira nyanja, ndi kuyambira ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko.

11. Iwenso, cifukwa ca mwazi wa pangano lako ndinaturutsa andende ako m'dzenje m'mene mulibe madzi.

12. Bwererani kudza kulinga, andende a ciyembekezo inu; ngakhale lero lino ndilalikira kuti ndidzakubwezera cowirikiza.

13. Pakuti ndadzikokera Yuda, ndadzaza uta ndi Efraimu; ndipo ndidzautsa ana ako, Ziyoni, alimbane nao ana ako, Yavani, ndipo ndidzakuyesa lupanga la ngwazi.

14. Ndipo Yehova adzaoneka pamwamba pao, ndi mubvi wace udzaturuka ngati mphezi; ndipo Ambuye Mulungu adzaomba lipenga, nadzayenda ndi akabvumvulu a kumwela.

15. Yehova wa makamu adzawacinjiriza; ndipo adzadza, nadzapondereza miyala yoponyera; ndipo adzamva, nadzacita phokoso ngati avinyo; ndipo adzadzazidwa ngati mbale, ngati ngondya za guwa la nsembe.

16. Ndipo Yehova Mulungu wao adzawapulumutsa tsiku ilo, ngati zoweta za anthu ace; pakuti adzakhala ngati miyala ya m'korona yakunyezimira pa dziko lace.

17. Pakuti ukoma wace ndi waukuru ndithu, ndi kukongola kwace nkwa kukuru ndithu! tirigu adzakometsera anyamata, ndi vinyo watsopano anamwali.

Werengani mutu wathunthu Zekariya 9