Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 9:9-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; pfuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini cipulumutso; wofatsa ndi wokwera pa buru, ndi mwana wamphongo wa buru.

10. Ndipo ndidzaononga magareta kuwacotsa m'Efraimu, ndi akavalo kuwacotsa m'Yerusalemu; ndi uta wa nkhondo udzaonongeka; ndipo adzanena zamtendere kwa amitundu; ndi ufumu wace udzakhala kuyambira kunyanja kufikira nyanja, ndi kuyambira ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko.

11. Iwenso, cifukwa ca mwazi wa pangano lako ndinaturutsa andende ako m'dzenje m'mene mulibe madzi.

12. Bwererani kudza kulinga, andende a ciyembekezo inu; ngakhale lero lino ndilalikira kuti ndidzakubwezera cowirikiza.

13. Pakuti ndadzikokera Yuda, ndadzaza uta ndi Efraimu; ndipo ndidzautsa ana ako, Ziyoni, alimbane nao ana ako, Yavani, ndipo ndidzakuyesa lupanga la ngwazi.

14. Ndipo Yehova adzaoneka pamwamba pao, ndi mubvi wace udzaturuka ngati mphezi; ndipo Ambuye Mulungu adzaomba lipenga, nadzayenda ndi akabvumvulu a kumwela.

15. Yehova wa makamu adzawacinjiriza; ndipo adzadza, nadzapondereza miyala yoponyera; ndipo adzamva, nadzacita phokoso ngati avinyo; ndipo adzadzazidwa ngati mbale, ngati ngondya za guwa la nsembe.

16. Ndipo Yehova Mulungu wao adzawapulumutsa tsiku ilo, ngati zoweta za anthu ace; pakuti adzakhala ngati miyala ya m'korona yakunyezimira pa dziko lace.

Werengani mutu wathunthu Zekariya 9