Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 9:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Katundu wa mau a Yehova pa dziko la Hadraki, ndipo Damasiko adzakhala popumula pace; pakuti Yehova apenyerera anthu monga apenyerera mafuko onse a Israyeli;

2. ndi Hamati yemwe wogundana naye malire; Turo ndi Zidoni, angakhale ali ndi nzeru zambiri.

3. Ndipo Turo adzadzimangira polimbikirapo, nadzakundika siliva ngati pfumbi, ndi golidi woyenga ngati thope la kubwalo.

4. Taonani, Yehova adzamlanda zace, nadzakantha mphamvu yace igwe m'manja; ndipo adzatha ndi moto.

5. Asikeloni adzaciona, nadzaopa; Gazanso, nadzanjenjemera kwambiri; ndi Ekroni, pakuti ciyembekezo cace cacitidwa manyazi; ndipo mfumu idzatayika ku Gaza, ndi Asikeloni adzasowa okhalamo.

6. Ndi mtundu wa anthu osokonezeka udzakhala m'Asidodi, ndipo ndidzaononga kudzikuza kwa Afilisti.

7. Ndipo ndidzacotsa mwazi wace m'kamwa mwace, ndi zonyansa zace pakati pa mano ace; momwemo iyenso adzakhala wotsalira wa Mulungu wathu, ndipo adzakhala ngati mkuru wa pfuko m'Yuda, ndi Ekroni ngati Myebusi.

8. Ndipo ndidzamangira nyumba yanga misasa, kuiletsera nkhondo, asapitepo munthu kapena kubweranso; ndipo wakuwasautsa sadzapitanso pakati pao; pakuti tsopano ndapenya ndi maso anga.

9. Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; pfuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini cipulumutso; wofatsa ndi wokwera pa buru, ndi mwana wamphongo wa buru.

10. Ndipo ndidzaononga magareta kuwacotsa m'Efraimu, ndi akavalo kuwacotsa m'Yerusalemu; ndi uta wa nkhondo udzaonongeka; ndipo adzanena zamtendere kwa amitundu; ndi ufumu wace udzakhala kuyambira kunyanja kufikira nyanja, ndi kuyambira ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko.

Werengani mutu wathunthu Zekariya 9