Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 8:17-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. ndipo musalingirira coipa m'mtima mwanu yense pa mnzace; nimusakonde lumbiro lonama; pakuti izi zonse ndidana nazo, ati Yehova.

18. Ndipo mau a Yehova wa makamu anadza kwa ine, ndi kuti,

19. Atero Yehova wa makamu: Kusala kwa mwezi wacinai, ndi kusala kwa mwezi wacisanu, ndi kusala kwa mwezi wacisanu ndi ciwiri, ndi kusala kwa mwezi wakhumi kukhale kwa nyumba ya Yuda cimwemwe ndi cikondwerero, ndi nyengo zoikika zosekerera; cifukwa cace kondani coonadi ndi mtendere.

20. Atero Yehova wa makamu: Kudzacitikanso kuti mitundu ya anthu, ndi okhalamo m'midzi yambiri adzafika,

21. ndi okhala m'mudzi umodzi adzamuka ku mudzi wina, ndi kuti, Tiyeni msanga kukapepeza Yehova, ndi kufunafuna Yehova wa makamu; ndimuka inenso.

22. Inde, mitundu yambiri ya anthu, ndi amitundu amphamvu adzadza kufunafuna Yehova wa makamu m'Yerusalemu, ndi kupepeza Yehova.

23. Atero Yehova wa makamu: Kudzacitika masiku awo amuna khumi adzagwira, ndiwo a manenedwe onse a amitundu, inde adzagwira mkawo wa munthu ali Myuda, ndi kuti, Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.

Werengani mutu wathunthu Zekariya 8