Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 7:9-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Watero Yehova wa makamu, kuti, Weruzani ciweruzo coona, nimucitire yense mnzace cifundo ndi ukoma mtima;

10. musazunza mkazi wamasiye, kapena ana amasiye, mlendo kapena waumphawi; ndipo nnena mmodzi wa inu alingirire m'mtima mwace kumcitira coipa munthu mnzace.

11. Koma anakana kumvera, nakaniza phewa lao, natseka makutu ao, kuti asamve.

12. Inde, anasanduliza mitima yao ikhale ngati mwala woti gwa, kuti angamve cilamulo, ndi mau amene Yehova wa makamu anatumiza ndi Mzimu wace mwa aneneri oyamba aja; m'menemo munafuma mkwiyo waukuru wocokera kwa Yehova wa makamu.

13. Ndipo kunacitika, monga Iye anapfuula, koma iwo sanamvera; momwemo iwo adzapfuula, koma Ine sindidzamva, ati Yehova wa makamu;

Werengani mutu wathunthu Zekariya 7