Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 6:10-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Tenga a iwo a kundende, a Keledai, a Tobiya, ndi a Yedaya; nudze tsiku lomwelo, nulowe ku nyumba ya Yosiya, mwana wa Zefaniya, kumene anafikirako kucokera ku Babulo,

11. ndipo utenge siliva ndi golidi, nupange akorona, nuwaike pamutu pa Yoswa mwana wa Yehozadaki mkuru wa ansembe;

12. nunene naye, kuti, Atero Yehova wa makamu, ndi kuti, Taonani, munthu dzina lace ndilo Mphukira, ndipo adzaphuka m'malo mwace, nadzamanga Kacisi wa Yehova:

Werengani mutu wathunthu Zekariya 6