Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 6:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anaturuka magareta anai pakati pa mapiri awiri; ndi mapiriwo ndiwo mapiri amkuwa.

2. Ku gareta woyamba kunali akavalo ofiira; ndi ku gareta waciwiri akavalo akuda;

3. ndi ku gareta wacitatu akavalo oyera; ndi ku gareta wacinai akavalo olimba amawanga.

4. Ndipo ndinayankha ndinati kwa mthenga wolankhula ndi ine, Izi nziani, mbuyanga?

5. Ndi mthenga anayankha, nati kwa ine, Izi ndi mphepo zinai zakumwamba zakuturuka kumene zimaimirira pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi.

6. Gareta wa akavalo akuda aturukira ku dziko la kumpoto; ndi oyerawo aturukira kuwatsata; ndi amawanga aturukira ku dziko la kumwela.

Werengani mutu wathunthu Zekariya 6