Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Zekariya 11:12-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo ndinanena nao, Cikakomera inu, ndipatseni mphotho yanga; ngati iai, lekani. Ndipo anayesa mphotho yanga, kulemera kwace ndarama zasiliva makumi atatu.

13. Ndipo Yehova anati kwa ine, Kaziponye kwa woumba mbiya, mtengo wace wokometsetsa anandiyesawo. Ndipo ndinatenga ndarama makumi atatu asiliva, ndi kuziponya kwa woumba mbiya, m'nyumba ya Yehova.

14. Pamenepo ndinadula ndodo yanga yina, ndiyo Comanganitsa, kuti ndithetse cibale ca pakati pa Yuda ndi Israyeli.

15. Ndipo Yehova anati kwa ine, Dzitengerenso zipangizo za mbusa wopusa.

16. Pakuti taonani, ndidzautsa mbusa m'dziko amene sadzazonda otayika, kapena kufunafuna zomwazika, kapena kulunzitsa yotyoka, kapena kudyetsa yamoyo, koma adzadya nyama ya zonenepa, nadzang'amba ziboda zao.

17. Tsoka mbusa wopanda pace, wakusiya zoweta! lupanga pa dzanja lace, ndi pa diso lace la kumanja; dzanja lace lidzauma konse, ndi diso lace lamanja lidzada bii.

Werengani mutu wathunthu Zekariya 11