Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoweli 3:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pakuti taonani, masiku awo, ndi nthawi iyo, pamene ndibwera nao andende a Yuda ndi a Yerusalemu,

2. ndidzasonkhanitsa amitundu onse, ndi kutsikira nao ku cigwa ca Yosafati; ndipo ndidzaweruzana nao komweko za anthu anga, ndi colowa canga Israyeli, amene anawabalalitsa mwa amitundu, nagawa dziko langa,

3. Ndipo anacitira anthu anga maere, napereka mwana wamwamuna kusinthana ndi mkazi wadama, nagula vinyo ndi mwana wamkazi kuti amwe.

4. Ndiponso ndiri ndi ciani ndi inu, Turo ndi Zidoni, ndi malire onse a Afilisti? mudzandibwezera cilango kodi? Mukandibwezera cilango msanga, mofulumira, ndidzabwezera cilango canu pamutu panu,

5. Popeza inu munatenga siliva wanga ndi golidi wanga, ndi kulonga zofunika zanga zokoma m'akacisi anu;

6. munagulitsanso ana a Yuda ndi ana a Yerusalemu kwa ana a Yavani, kuwacotsa kutali kwa malire ao;

Werengani mutu wathunthu Yoweli 3