1. Muombe lipenga m'Ziyoni, nimupfuulitse m'phiri langa lopatulika; onse okhala m'dziko anjenjemere; pakuti tsiku la Yehova lirinkudza, pakuti liyandikira;
2. tsiku la mdima, la mdima wandiweyani, tsiku la mitambo, mitambo yocindikira, ngati m'mbandakuca moyalika pamapiri; mtundu waukuru ndi wamphamvu, panalibe wotere ndi kale lonse, sipadzakhalanso wotere utapita uwu, kufikira zaka za mibadwo yambiri.
3. Moto unyambita pamaso pao, ndi m'mbuyo mwao litentha lawi la moto; kumaso kwao dziko likunga munda wa Edeni, koma m'mbuyo mwao likunga cipululu copanda kanthu; palibenso wakuwapulumuka.
4. Maonekedwe ao aoneka ngati akavalo, nathamanga ngati akavalo a nkhondo.
5. Atumphako ngati mkokomo wa magareta pamwamba pa mapiri, ngati kulilima kwa malawi a moto akupsereza ziputu, ngati mtundu wamphamvu wa anthu ondandalikira nkhondo.
6. Pamaso pao mitundu ya anthu ikumva zowawa, nkhope zonse zitumbuluka.
7. Athamanga ngati amphamvu; akwera linga ngati anthu a nkhondo; niliyenda liri lonse njira yace, osasokonezeka m'mabande ao.
8. Sakankhana, ayenda liri lonse m'mopita mwace; akagwa m'zida, siityoka nkhondo yao.