Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoweli 1:15-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Kalanga ine, tsikuli! pakuti layandikira tsiku la Yehova, lidzafika ngati cionongeko cocokera kwa Wamphamvuyonse.

16. Cakudya sicicotsedwa kodi pamaso pathu? cimwemwe ndi cikondwerero pa nyumba ya Mulungu wathu?

17. Mbeu zaola pansi pa zibuluma zao; zosungiramo zaonongeka, nkhokwe zapasuka; pakuti tirigu wakwinyata.

18. Ha! nyama ziusa moyo, magulu a ng'ombe azimidwa; pakuti zisowa podyera; magulu a nkhosa omwe atha.

19. Ndipfuulira kwa Inu Yehova, pakuti moto wapsereza mabusa a m'cipululu, ndi malawi a moto anatentha mitengo yonse ya kuthengo,

20. inde nyama za kuthengo zilira kwa Inu; pakuti mitsinje yamadzi yaphwa, ndi moto wapsereza mabusa a m'cipululu.

Werengani mutu wathunthu Yoweli 1