Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoweli 1:13-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Mudzimangire ciguduli m'cuuno mwanu, nimulire ansembe inu; bwnani, otumikira ku guwa la nsembe inu; lowani, gonani usiku wonse m'ciguduli, inu otumikira Mulungu wanga; pakuti nsembe yaufa ndi nsembe yothira zaletsedwera nyumba ya Mulungu wanu.

14. Patulani tsiku losala, lalikirani masonkhano oletsa, sonkhanitsani akulu akulu, ndi onse okhala m'dziko, ku nyumba ya Yehova Mulungu wanu; nimupfuulire kwa Yehova.

15. Kalanga ine, tsikuli! pakuti layandikira tsiku la Yehova, lidzafika ngati cionongeko cocokera kwa Wamphamvuyonse.

16. Cakudya sicicotsedwa kodi pamaso pathu? cimwemwe ndi cikondwerero pa nyumba ya Mulungu wathu?

17. Mbeu zaola pansi pa zibuluma zao; zosungiramo zaonongeka, nkhokwe zapasuka; pakuti tirigu wakwinyata.

Werengani mutu wathunthu Yoweli 1