Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 9:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yoswa anyengedwa ndi Agibeoni napangana nao. Ndipo kunali, pakumva ici mafumu onse a tsidya ilo la Yordano, kumapiri ndi kucidikha, ndi ku madoko onse a nyanja yaikuru, pandunji pa Lebano: Ahiti ndi Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi;

2. anasonkhana kuponyana ndi Yoswa ndi Israyeli, ndi mtima umodzi.

3. Koma pamene nzika za Gibeoni zinamva zimene Yoswa adacitira Yeriko ndi Ai,

4. zinacita momcenierera, nizimuka nizioneka ngati mithenga, nizitenga matumba akale pa aburu ao, ndi matumba a vinyo akale ndi ong'ambika ndi omangamanga;

5. ndi nsapato zakale za zigamba pa mapazi ao, nizibvala nsanza; ndi mikate yonse ya kamba wao inali youma ndi yoyanga nkhungu.

6. Ndipo zinamuka kwa Yoswa kumisasa ku Giligala, niziti kwa iye ndi kwa amuna a Israyeli, Tacokera dziko lakutali, cifukwa cace mupangane nafe.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 9