Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 4:10-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Pakuti ansembe akusenza likasa anaima pakati pa Yordano, mpaka zitatha zonse Yehova adazilamulira Yoswa anene kwa anthu, monga mwa zonse Mose adalamulira Yoswa; ndipo anthu anafulumira kuoloka.

11. Ndipo kunali, atatha kuoloka anthu onse, likasa la Yehova linaoloka, ndi ansembe, pamaso pa anthu.

12. Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi gawo lija la pfuko la Manase anaoloka ndi zida zao pamaso pa ana a Israyeli, monga Mose adanena nao;

13. ngati zikwi makumi anai ankhondo okonzeka anaoloka pamaso pa Yehova kuthira nkhondo ku zidikha za Yeriko.

14. Tsiku lomwelo Yehova anakulitsa Yoswa pamaso pa Aisrayeli onse; ndipo anamuopa monga anaopa Mose, masiku onse amoyowace.

15. Ndipo Yehova anati kwa Yoswa,

16. Lamulira ansembe akusenza likasa la umboni, kuti akwere kuturuka m'Yordano.

17. Pamenepo Yoswa analamulira ansembe, ndi kuti, Kwerani kuturuka m'Yordano.

18. Ndipo kunali, atakwera ansembe akusenza likasa la cipangano la Yehova, kuturuka pakati pa Yordano, nakwera pamtunda mapazi a ansembe, madzi a m'Yordano anabwera m'njira mwace, nasefuka m'magombe ace onse monga kale.

19. Ndipo anthu anakwera kuturuka m'Yordano tsiku lakhumi la mwezi woyamba, namanga misasa ku Giligala, mbali ya ku m'mawa kwa Yeriko.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 4