Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 3:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yoswa analawirira mamawa, kucoka ku Sitimu, nafika ku Yordano, iye ndi ana onse a Israyeli; nagona komweko, asanaoloke.

2. Ndipo kunali atapita masiku atatu, akapitao anapita pakati pa cigono;

3. nalamulira anthu, ndi kuti, Mukadzaona likasa la cipangano la Yehova Mulungu wanu, ndi ansembe Aleviwo atalisenza, pamenepo mucoke kwanu ndi kulitsata.

4. Koma pakhale dera pakati pa inu ndi ilo, monga mikono zikwi ziwiri poliyesa; musaliyandikire, kuti mudziwe njira imene muziyendamo; popeza simunapita njirayi kufikira lero.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 3