Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 23:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo atapita masiku ambiri, Yehova atapumulitsa Israyeli kwa adani ao onse akuwazungulira, ndipo Yoswa adakalamba nakhala wa zaka zambiri;

2. Yoswa anaitana Aisrayeli onse, akulu akulu ao, ndi akuru ao, ndi oweruza ao, ndi akapitao ao, nanena nao, Ndakalamba, ndine wa zaka zambiri;

3. ndipo munapenya zonse Yehova Mulungu anacitira mitundu iyi yonse ya anthu cifukwa ca inu; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye anakuthirirani nkhondo.

4. Taonani, ndakugawirani mitundu ya anthu iyi yotsala ikhale colowa ca mapfuko anu, kuyambira ku Yordano, ndi mitundu yonse ya anthu ndinaipasula, mpaka ku nyanja yaikuru ku malowero a dzuwa.

5. Ndipo Yehova Mulungu wanu Iyeyu adzawapitikitsa pamaso panu, ndi kulanda dziko lao kuwacotsa pamaso panu, ndipo mudzalandira dziko lao likhale colowa canu; monga Yehova Mulungu wanu ananena ndi inu.

6. Koma mulimbike mtima kwambiri kusunga ndi kucita zonse zolembedwa m'buku la cilamulo ca Mose, osacipambukira kulamanja kapena kulamanzere;

7. osalowa pakati pa amitundu awa otsala mwa inu; kapena kuchula dzina la milungu yao; osalumbiritsa nalo, kapena kuitumikira, kapena kuigwadira;

8. koma muumirire Yehova Mulungu wanu, monga munacita mpaka lero lino.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 23