Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 21:6-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo ana a Gerisoni analandira molota maere motapa pa mabanja a pfuko la Isakara, ndi pa pfuko la Aseri, ndi pa pfuko la Nafitali, ndi pa pfuko la Manase logawika pakati m'Basana, midzi khumi ndi itatu.

7. Ana a Merari, monga mwa mabanja ao, analandira motapa pa pfuko la Rubeni, ndi pa pfuko la Gadi, ndi pa pfuko la Zebuloni midzi khumi ndi iwiri.

8. Motero ana a Israyeli anapatsa Alevi midzi iyi ndi mabusa ao, molota maere, monga Yehova adalamulira mwa dzanja la Mose.

9. Ndipo anapatsa motapa pa pfuko la ana a Yuda, ndi pa pfuko la ana a Simeoni, midzi iyi yochulidwa maina ao;

10. kuti ikhale ya ana a Aroni a mabanja a Akohati, a ana a Levi, pakuti maere oyamba adaturukira iwowa.

11. Ndipo anawapatsa mudzi wa Ariba, ndiye atate wa Anoki, womwewo ndi Hebroni, ku mapiri a Yuda, ndi mabusa ace ozungulirapo.

12. Koma minda ya mudzi ndi miraga yace anapatsa Kalebe mwana wa Yefune, ikhale yace.

13. Ndipo kwa ana a Aroni wansembe anapatsa Hebroni ndi mabusa ace, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzace, ndi Libina ndi mabusa ace;

14. ndi Yatiri ndi mabusa ace, ndi Esitimoa ndi mabusa ace;

15. ndi Holoni ndi mabusa ace, ndi Debiri ndi mabusa ace;

16. ndi Aini ndi mabusa ace, ndi Yuta ndi mabusa ace, ndi Betisemesi ndi mabusa ace; midzi isanu ndi inai yotapira mapfuko awiri aja.

17. Ndipo motapira pfuko La Benjamini, Gibeoni ndi mabusa ace, Geba ndi mabusa ace,

18. Anatotu ndi mabusa ace, ndi Alimoni ndi mabusa ace; midzi inai.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 21