Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 21:6-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo ana a Gerisoni analandira molota maere motapa pa mabanja a pfuko la Isakara, ndi pa pfuko la Aseri, ndi pa pfuko la Nafitali, ndi pa pfuko la Manase logawika pakati m'Basana, midzi khumi ndi itatu.

7. Ana a Merari, monga mwa mabanja ao, analandira motapa pa pfuko la Rubeni, ndi pa pfuko la Gadi, ndi pa pfuko la Zebuloni midzi khumi ndi iwiri.

8. Motero ana a Israyeli anapatsa Alevi midzi iyi ndi mabusa ao, molota maere, monga Yehova adalamulira mwa dzanja la Mose.

9. Ndipo anapatsa motapa pa pfuko la ana a Yuda, ndi pa pfuko la ana a Simeoni, midzi iyi yochulidwa maina ao;

10. kuti ikhale ya ana a Aroni a mabanja a Akohati, a ana a Levi, pakuti maere oyamba adaturukira iwowa.

11. Ndipo anawapatsa mudzi wa Ariba, ndiye atate wa Anoki, womwewo ndi Hebroni, ku mapiri a Yuda, ndi mabusa ace ozungulirapo.

12. Koma minda ya mudzi ndi miraga yace anapatsa Kalebe mwana wa Yefune, ikhale yace.

13. Ndipo kwa ana a Aroni wansembe anapatsa Hebroni ndi mabusa ace, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzace, ndi Libina ndi mabusa ace;

14. ndi Yatiri ndi mabusa ace, ndi Esitimoa ndi mabusa ace;

Werengani mutu wathunthu Yoswa 21