Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 21:40-45 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

40. Yonseyi ndiyo midzi ya ana a Merari monga mwa mabanja ao, ndiwo otsala a mabanja a Alevi; ndipo gawo lao ndilo midzi khumi ndi iwiri.

41. Midzi yonse ya Alevi, pakati pa colowa ca ana a Israyeli ndiyo midzi makumi anai kudza isanu ndi itatu, ndi mabusa ao.

42. Midzi iyi yonse inali nao mabusa ao pozungulira pao: inatero midzi iyi yonse.

43. Motero Yehova anawapatsa Israyeli dziko lonse adalumbiralo kuwapatsa makolo ao: ndipo analilandira lao lao, nakhala m'mwemo.

44. Ndipo Yehova anawapatsa mpumulo pozungulira ponse, monga mwa zonse adalumbirira makolo ao; ndipo pamaso pao sipanaima munthu mmodzi wa adani ao onse; Yehova anapereka adani ao onse m'manja mwao.

45. Sikadasowa kanthu konse ka zinthu zokoma zonse Yehova adazinenera nyumba ya Israyeli; zidacitika zonse.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 21