36. Ndipo motapira pa pfuko la Rubeni, Bezeri ndi mabusa ace, ndi Yahazi ndi mabusa ace,
37. Kedimotu ndi mabusa ace, ndi Mefati ndi mabusa ace; midzi inai.
38. Ndipo motapira m'pfuko la Gadi, Ramoti m'Gileadi ndi mabusa ace ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzaceyo, ndi Mahanaimu ndi mabusa ace;
39. Hesiboni ndi mabusa ace. Yazeri ndi mabusa ace: yonse pamodzi midzi inai.
40. Yonseyi ndiyo midzi ya ana a Merari monga mwa mabanja ao, ndiwo otsala a mabanja a Alevi; ndipo gawo lao ndilo midzi khumi ndi iwiri.
41. Midzi yonse ya Alevi, pakati pa colowa ca ana a Israyeli ndiyo midzi makumi anai kudza isanu ndi itatu, ndi mabusa ao.
42. Midzi iyi yonse inali nao mabusa ao pozungulira pao: inatero midzi iyi yonse.
43. Motero Yehova anawapatsa Israyeli dziko lonse adalumbiralo kuwapatsa makolo ao: ndipo analilandira lao lao, nakhala m'mwemo.
44. Ndipo Yehova anawapatsa mpumulo pozungulira ponse, monga mwa zonse adalumbirira makolo ao; ndipo pamaso pao sipanaima munthu mmodzi wa adani ao onse; Yehova anapereka adani ao onse m'manja mwao.