1. Pamenepo akuru a nyumba za atate a Alevi anayandikira kwa Eleazare wansembe, ndi kwa Yoswa mwana wa Nuni, ndi kwa akuru a nyumba za atate a mapfuko a ana a Israyeli;
2. nanena nao ku Silo m'dziko la Kanani, ndi kuti Yehova analamulira mwa dzanja la Mose kuti atipatse midzi yokhalamo ife, ndi mabusa a zoweta zathu.
3. Ndipo ana a Israyeli anapatsa Alevi, kutapa pa colowa cao, monga mwa lamulo la Yehova, midzi iyi ndi mabusa ao.
4. Ndipo maere anaturukira mabanja a Akohati; ndipo molota maere ana a Aroni wansembe, ndiwo Alevi, analandira motapa pa pfuko la Yuda, ndi pa pfuko la Simeoni, ndi pa pfuko la Benjamini, midzi khumi ndi itatu.
5. Ndipo ana otsala a Kohati analandira molota maere motapa pa mabanja a pfuko la Efraimu, ndi pa pfuko La Dani, ndi pa pfuko La Manase logawika pakati, midzi khumi.
6. Ndipo ana a Gerisoni analandira molota maere motapa pa mabanja a pfuko la Isakara, ndi pa pfuko la Aseri, ndi pa pfuko la Nafitali, ndi pa pfuko la Manase logawika pakati m'Basana, midzi khumi ndi itatu.
7. Ana a Merari, monga mwa mabanja ao, analandira motapa pa pfuko la Rubeni, ndi pa pfuko la Gadi, ndi pa pfuko la Zebuloni midzi khumi ndi iwiri.
8. Motero ana a Israyeli anapatsa Alevi midzi iyi ndi mabusa ao, molota maere, monga Yehova adalamulira mwa dzanja la Mose.
9. Ndipo anapatsa motapa pa pfuko la ana a Yuda, ndi pa pfuko la ana a Simeoni, midzi iyi yochulidwa maina ao;