Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 2:18-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Taona, tikadzalowa m'dzikomo ife, uzimanga cingwe ici cofiira pazenera pamene watitsitsira; ndipo udzasonkhanitsa m'nyumbamo atate wako ndi mai wako nui abale ako ndi a m'nyumba onse a atate wako.

19. Ndipo kudzakhala kuti ali yense akadzaturuka pa khomo la nyumba yako kubwalo, imfa imeneyi ndi yace, tiribe kuparamula ife; koma ali yense adzakhala ndi iwe m'nyumba, likamfikira dzanja, imfa imeneyi ndi yathu.

20. Koma ukaulula codzera ifeco tidzamasukira lumbiro lako watilumbiritsali.

21. Nati iye, Momwemo, monga mwa mau anu. Ndipo anawauza amuke, iwo namuka; namanga iye cingwe cofiiraco pazenera.

22. Ndipo anayenda iwo, nafika kuphiri, nakhalako masiku atatu mpaka atabwerera olondolawo; popeza olondolawo anawafunafuna panjira ponse, osawapeza.

23. Pamenepo amuna awiriwo anabwerera, natsika m'phirimo naoloka, nafika kwa Yoswa mwana wa Nuni, namfotokozera zonse zidawagwera.

24. Ndipo anati kwa Yoswa, Zoonadi, Yehova wapereka dziko lonse m'manja mwathu; ndiponso nzika zonse zasungunuka pamaso pathu.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 2