Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 2:12-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo tsopano, mundilumbiriretu kwa Yehova, popeza ndakucitirani cifundo, kuti inunso mudzacitira cifundo a m'nyumba ya atate wanga ndi kundipatsa cizindikilo coona,

13. kuti mudzawasunga ndi moyo atate wanga ndi mai wanga, ndi alongo anga ndi abale anga, ndi zonse ali nazo, ndi kupulumutsa miyoyo yathu kuimfa.

14. Ndipo amunawo anati kwa iye, Moyo wathu ndiwo moyo wanu, mukapanda kuulula codzera ife; ndipo kudzakhala kuti, pakutipatsa ife dziko ili Yehova, tidzakucitira cifundo ndi coonadi.

15. Pamenepo anawatsitsa pazenera ndi cingwe; popeza nyumba yace lnali pa linga La mudzi, nakhala iye palingapo.

16. Ndipo anati kwa iwo, Mukani kuphiri, olondola angakupezeni; mubisale kumeneko masiku atatu, mpaka atabwerera olondolawo, pamenepo muyende ulendo wanu.

17. Ndipo amunawo anati kwa iye, Sitidzacimwira lumbiro lako ili watilumbiritsali.

18. Taona, tikadzalowa m'dzikomo ife, uzimanga cingwe ici cofiira pazenera pamene watitsitsira; ndipo udzasonkhanitsa m'nyumbamo atate wako ndi mai wako nui abale ako ndi a m'nyumba onse a atate wako.

19. Ndipo kudzakhala kuti ali yense akadzaturuka pa khomo la nyumba yako kubwalo, imfa imeneyi ndi yace, tiribe kuparamula ife; koma ali yense adzakhala ndi iwe m'nyumba, likamfikira dzanja, imfa imeneyi ndi yathu.

20. Koma ukaulula codzera ifeco tidzamasukira lumbiro lako watilumbiritsali.

21. Nati iye, Momwemo, monga mwa mau anu. Ndipo anawauza amuke, iwo namuka; namanga iye cingwe cofiiraco pazenera.

22. Ndipo anayenda iwo, nafika kuphiri, nakhalako masiku atatu mpaka atabwerera olondolawo; popeza olondolawo anawafunafuna panjira ponse, osawapeza.

23. Pamenepo amuna awiriwo anabwerera, natsika m'phirimo naoloka, nafika kwa Yoswa mwana wa Nuni, namfotokozera zonse zidawagwera.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 2