1. NDIPO atafa Mose mtumiki wa Yehova, Yehova anati kwa Yoswa mwana wa Nuni mnyamata wa Mose,
2. Mose mtumiki wanga wafa; tauka tsono, nuoloke Yordano uyu, iwe ndi anthu awa onse, kulowa m'dzikomo ndirikuwapatsa, ndiwo ana a Israyeli.
3. Pali ponse phazi lanu lidzapondapo ndinakupatsani, monga ndinanena ndi Mose.