Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yona 1:5-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Pamenepo amarinyero anacita mantha, napfuulira yense kwa mlungu wace, naponya m'nyanja akatundu anali m'combo kucipepuza. Koma Yona adatsikira m'munsi mwa combo, nagona tulo tofa nato.

6. Ndipo mwini combo anadza kwa iye, nanena naye, Utani iwe wam'tulo? uka, itana Mulungu wako, kapena Mulunguyo adzatikumbukila tingatayike.

7. Ndipo anati yense kwa mnzace, Tiyeni ticite maere, kuti tidziwe coipa ici catigwera cifukwa ca yani. M'mwemo anacita maere, ndipo maere anagwera Yona.

8. Pamenepo anati kwa iye, Utiuzetu coipa ici catigwera cifukwa ca yani? nchito yako njotani? ufuma kuti? dziko lako nliti? nanga mtundu wako?

9. Ndipo ananena nao, Ndine Mhebri, ndiopa Yehova Mulungu wa Kumwamba amene analenga nyanja ndi mtunda.

10. Pamenepo amunawo anaopa kwambiri, nati kwa iye, Ici nciani wacicita? Pakuti amunawo anadziwa kuti anathawa pamaso pa Yehova, popeza adawauza.

11. Tsono anati kwa iye, Ticitenji nawe, kuti nyanja iticitire bata? popeza namondwe anakula-kulabe panyanja.

12. Ndipo anati nao, Mundinyamule ndi kundiponya m'nyanja, momwemo nyanja idzacitira inu bata; pakuti ndidziwa kuti namondwe wamkuru amene wakugwerani cifukwa ca ine.

13. Koma amunawo anapalasa kubwerera kumtunda, koma sanathe; pakuti namondwe wa panyanja anakulakula mokomana nao.

14. Pamenepo anapfuulira kwa Yehova, nati, Tikupemphanitu, Yehova, tisatayike cifukwa ca moyo wa munthu uyu, musatisenzetse mwazi wosacimwa; pakuti, Inu Yehova, mwacita monga mudakomera Inu.

15. Momwemo ananyamula Yona, namponya m'nyanja; ndipo nyanja inaleka kukokoma kwace.

16. Ndipo amunawo anaopa Yehova ndi manthaakuru, namphera Yehova nsembe, nawinda.

17. Koma Yehova anaikiratu cinsomba cacikuru cimeze Yona; ndipo Yona anali m'miroba mwa nsombayi masiku atatu usana ndi usiku.

Werengani mutu wathunthu Yona 1