Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 9:4-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndiye wa mtima wanzeru, ndi wa mphamvu yaikuru;Ndaniyo anadziumitsa mtima pa Iye, nakhala nao mtendere?

5. Ndiye amene asuntha mapiri, osacidziwa iwo,Amene amagubuduza mu mkwiyo wace.

6. Amene agwedeza dziko lapansi licoke m'malo mwace,Ndi mizati yace injenjemere.

7. Amene alamulira dzuwa ndipo silituruka,Nakomera nyenyezi cizindikilo cakuzitsekera.

8. Woyala thambo yekha,Naponda pa mafunde a panyanja.

9. Wolenga Mlalang'amba, Akamwiniatsatana, ndi Nsangwe,Ndi Kumpotosimpita,

10. Wocita zazikuru zosasanthulika,Ndi zodabwiza zosawerengeka,

11. Taona, Mulungu apita pali ine, koma sindimpenya;Napitirira, koma osamaindikira ine.

12. Taona, akwatula, adzambwezetsa ndani?Adzanena naye ndani, Mulikucita ciani?

13. Mulungu sadzabweza mkwiyo wace;Athandizi odzikuza awerama pansi pa Iye.

Werengani mutu wathunthu Yobu 9