Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 9:23-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Mkwapulo ukapha modzidzimutsa,Adzaseka tsoka la wosacimwa.

24. Dziko lapansi laperekedwa m'dzanja la woipa;Aphimba maso a oweruza ace.Ngati sindiye, pali yaninso?

25. Tsopano masiku anga afulumira kuposa wamtokoma;Athawa osaona cokoma.

26. Apitirira ngati zombo zaliwiro;Ngati mphungu igudukira cakudya cace.

27. Ndikati, Ndidzaiwala condidandaulitsa,Ndidzasintha nkhope yanga yacisoni, ndidzasekerera;

28. Pamenepo ndiopa zisoni zanga zonse,Ndidziwa kuti simudzandiyesa wosacimwa.

29. Mlandu udzanditsutsa;Potero ndigwire nchito cabe cifukwa ninji?

30. Ndikasamba madzi a cipale cofewaNdi kuyeretsa manja anga ndi sopo;

31. Mudzandibviikanso muli zoola,Ndi zobvala zanga zidzanyansidwa nane.

32. Pakuti sindiye munthu, monga ine, kuti ndimyankhe,Kuti tikomane mlandu.

33. Palibe wakutiweruza,Wakutisanjika ife tonse awiri manja ace.

34. Andicotsere ndodo yace,Coopsa cace cisandicititse mantha;

35. Kuti ndinene, osamuopa,Pakuti sinditero monga umo ndiri.

Werengani mutu wathunthu Yobu 9